2 Corinthians 8:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zonse mudalandira pakulu, monga kukhulupirira, kulankhula, kudziŵa zinthu, kuchita changu pa zonse, ndiponso kutikonda. Motero tifuna kuti muperekenso pakulu zachifundozi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma monga muchulukira m'zonse, m'chikhulupiriro, ndi m'mau, ndi m'chidziwitso, ndi m'khama lonse, ndi m'chikondi chanu cha kwa ife, chulukaninso m'chisomo ichi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza pa zinthu zonse munachita bwino, monga pachikhulupiriro, poyankhula, pachidziwitso, pakhama lambiri ndi pachikondi chanu pa ife, onetsetsani kuti muchitenso bwino pachisomo ichi chopereka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma monga mucurukira m'zonse, m'cikhulupiriro, ndi m'mau, ndi m'cidziwitso, ndi m'khama lonse, ndi m'cikondi canu ca kwa ife, curukaninso m'cisomo ici.