2 Corinthians 9:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zoonadi ntchito imeneyi yomwe mukuchitira anthu a Mulungu, siingoŵathandiza pa zosoŵa zao, komanso chotsatira chake china nchakuti anthu ochuluka adzathokoza Mulungu kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za oyera mtima zokha, koma uchulukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ntchito imene mukugwirayi siyongothandiza kokha anthu a Mulungu kupeza zosowa, komanso ikuthandiza kuti anthu ambiri ayamike Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti utumiki wa kutumikira kumene sudzaza zosowa za oyera mtima zokha, koma ucurukiranso kwa Mulungu mwa mayamiko ambiri;