2 Corinthians 9:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti ntchito imeneyi ikuŵatsimikizira kuti chifundo chanu nchoona, iwo adzatamanda Mulungu chifukwa cha kumvera kwanu povomereza Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Adzatero chifukwanso cha ufulu wanu poŵagaŵirako iwowo ndi anthu ena onse zinthu zimene muli nazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza kuti mwa kuyesa kwa utumiki umene alemekeza Mulungu pa kugonja kwa chivomerezo chanu ku Uthenga Wabwino wa Khristu, ndi kwa kuolowa manja kwa chigawano chanu kwa iwo ndi kwa onse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha ntchito imene mwawatsimikizira nokha, anthu ena onse adzayamika Mulungu chifukwa cha kumvera kwanu kumene kumaonekera pamene mukuvomereza Uthenga Wabwino wa Khristu, ndiponso chifukwa chowagawira mowolowamanja iwowo pamodzi ndi wina aliyense.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza kuti mwa kuyesa kwa utumiki umene alemekeza Mulungu pa kugonia kwa cibvomerezo canu ku Uthenga Wabwino wa Kristu, ndi kwa kuolowa manja kwa cigawano canu kwa iwo ndi kwa onse;