2 Corinthians 9:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikudziŵa kuti mumafunadi kuthandiza, ndipo ndimakunyadirani kwa anthu a ku Masedoniya chifukwa cha chimenechi. Ndimaŵauza kuti, “Abale a ku Akaiya adakonzeka kale chaka chatha kuti athandize.” Ndipo changu chanu chautsa ena ambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti ndidziwa chivomerezo chanu chimene ndidzitamandira nacho chifukwa cha inu ndi Amasedoniya, kuti Akaya anakonzekeratu chitapita chaka; ndi changu chanu chinautsa ochulukawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza ndikudziwa mtima wanu wofuna kuthandiza, ndipo ndakhala ndikuwawuza monyadira a ku Makedoniya za chimenechi. Ndimawawuza kuti inu a ku Akaya munakonzeka kale chaka chatha kuti mupereke. Ndipo changu chanu chapatsa chidwi ambiri mwa iwo kuti nawonso achitepo kanthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti ndidziwa cibvomerezo canu cimene ndidzitamandira naco cifukwa ca inu ndi Amakedoniya, kuti Akaya anakonzekeratu citapita caka; ndi cangu canu cinautsa ocurukawo.