2 Corinthians 9:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake ndidaganiza kuti ndiyenera kupempha abale ameneŵa kuti abwere kwa inu ndisanafike ineyo, ndipo kuti akonzeretu mphatso imene mudalonjeza kale. Pamenepo mphatsoyo idzakhala yokonzekeratu, ndipo idzakhaladi mphatso yeniyeni, osati kanthu kamene mwapereka mokakamizidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake ndinayesa kuti kufunika kupempha abale kuti atsogole afike kwa inu, nakonzeretu dalitso lanu lolonjezeka kale, kuti chikhale chokonzeka chomwechi, monga ngati mdalitso, ndipo si monga mwa kuumiriza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ndinaganiza kuti nʼkofunika kupempha abale kuti adzakuchezereni ineyo ndisanafike, ndikuti adzatsirize kukonzekera mphatso zomwe munalonjeza kupereka mowolowamanja. Motero mphatsoyo idzakhala yokonzeratu, ndipo idzakhala mphatso yoperekedwa mowolowamanja, osati mokakamizidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ndinayesa kuti kufunika kupempha abale kuti atsogole afike kwa inu, nakonzeretu dalitso lanu lolonjezeka kale, kuti cikhale cokonzeka comweci, monga ngati mdalitso, ndipo si monga mwa kuumiriza.