2 John 1:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndili ndi zambiri zoti ndikuuzeni, koma sindifuna kuzilemba m'kalata. Ndikuyembekeza kubwera kwanuko kuti tidzakambirane pakamwa mpakamwa. Pamenepo chimwemwe chathu chidzakhala chathunthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pokhala ndili nazo zambiri zakukulemberani, sindifuna kuchita ndi kalata ndi kapezi; koma ndiyembekeza kudza kwa inu, ndi kulankhula popenyana, kuti chimwemwe chanu chikwanire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndili nazo zambiri zoti ndikulembereni, koma sindikufuna kuzilemba mʼkalata. Mʼmalo mwake, ndikuyembekeza kufika kwanuko kuti tidzakambirane nanu pamaso ndi pamaso, potero chimwemwe chathu chidzakhala chathunthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pokhala ndiri nazo zambiri zakukulemberani, sindifuna kucita ndi kalata ndi kapezi; koma ndiyembekeza kudza kwa inu, ndi kulankhula popenyana, kuti cimwemwecanucikwanire.