2 John 1:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye tsopano ndikukupemphani mai: tizikondana. Pakutero sindikukulemberani lamulo latsopano ai, koma lomwe lija limene takhala nalo kuyambira pa chiyambi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano ndikupemphani, mkazi womveka inu, wosati monga kukulemberani lamulo latsopano, koma lomwelo tinali nalo kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo tsopano, amayi wokondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano koma lomwe lija takhala nalo kuyambira pachiyambi. Ine ndikukupemphani kuti tidzikondana wina ndi mnzake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano ndikupemphani, mkazi womveka inu, wosati monga kukulemberani lamulo latsopano, koma lomwelo tinali nalo kuyambira paciyambi, kuti tikondane wina ndi mnzace.