2 John 1:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chikondi chimene ndikunenachi nchakuti tikhale omvera malamulo a Mulungu. Lamulo limene ndikukulemberanilo, monga mudamva kuyambira pa chiyambi, ndi lakuti moyo wanu uzikhala wachikondi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chikondi ndi ichi, kuti tiyende monga mwa malamulo ake. Ili ndi lamulolo, monga mudalimva kuyambira pachiyambi, kuti mukayende momwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo chikondi ndiye kuyenda momvera malamulo ake. Lamulo lake ndi lakuti mukhale moyo wachikondi monga munamva kuyambira pachiyambi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cikondi ndi ici, kuti tiyende monga mwa malamulo ace. Ili ndi lamulolo, monga mudalimva kuyambira paciyambi, kuti mukayende momwemo.