2 John 1:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja pakuwoneka anthu ambiri onyenga pa dziko lapansi. Iwo savomereza kuti Yesu Khristu adadzakhaladi munthu. Munthu wosavomereza zimenezi ndi wonyenga, ndiponso woukira Khristu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti onyenga ambiri adatuluka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikunena zimenezi chifukwa anthu ambiri onyenga, amene savomereza kuti Yesu Khristu anabwera monga munthu, akuyenda mʼdziko lapansi. Munthu aliyense otere ndi wonyenga ndiponso wokana Khristu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti onyenga ambiri adaturuka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene sabvomereza kuti Yesu Kristu anadza m'thupi, Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Kristu.