2 Kings 1:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Eliya adauza mkulu wa ankhondo makumi asanu aja kuti, “Ngati ine ndinedi munthu wa Mulungu, moto utsike kumwamba, ukupsereze iweyo pamodzi ndi anthu ako makumi asanuŵa.” Pomwepo moto udatsikadi kumwamba, nupsereza mkuluyo pamodzi ndi anthu ake makumi asanuwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nayankha Eliya, nanena ndi mtsogoleriyo, Ndikakhala ine munthu wa Mulungu, utsike moto wakumwamba, nunyeketse iwe ndi makumi asanu ako. Pamenepo unatsika moto kumwamba, nunyeketsa iye ndi makumi asanu ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Eliya anayankha mtsogoleriyo kuti, “Ngati ndine munthu wa Mulungu, moto utsike kuchokera kumwamba, ukupsereze iwe pamodzi ndi anthu makumi asanu akowo!” Pomwepo moto unatsikadi kuchokera kumwamba ndipo unapsereza mtsogoleriyo pamodzi ndi anthu akewo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nayankha Eliya, nanena ndi mtsogoleriyo, Ndikakhala ine munthu wa Mulungu, utsike mota wakumwamba, nunyeketse iwe ndi makumi asanu ako. Pamenepo unatsika mota kumwamba, nunyeketsa iye ndi makumi asanu ace.