2 Kings 1:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumu idatumanso mkulu wina pamodzi ndi ankhondo ake makumi asanu. Mkuluyo ndi anthu ake adapita, nakauza Eliya uja kuti, “Inu munthu wa Mulungu, mfumu ikukulamulani kuti mutsike msanga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anabwereza kutuma kwa iye mtsogoleri wina ndi makumi asanu ake. Ndipo iye anayankha nanena naye, Munthu wa Mulungu iwe, itero mfumu, Tsika msanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zitachitika izi, mfumu inatumanso mtsogoleri wina pamodzi ndi asilikali ake makumi asanu. Mtsogoleriyo anati kwa Eliya, “Munthu wa Mulungu, zimene mfumu ikunena ndi izi, ‘Tsikani msangamsanga!’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anabwereza kutuma kwa iye mtsogoleri wina ndi makumi asanu ace. Ndipo iye anayankha nanena naye, Munthu wa Mulungu iwe, itero mfumu, Tsika msanga.