2 Kings 1:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Eliya adamuyankha kuti, “Ngati ine ndinedi munthu wa Mulungu, moto utsike kumwamba, ukupsereze iweyo pamodzi ndi anthu ako makumi asanuŵa.” Pomwepo moto wa Mulungu udatsikadi kumwamba, nupsereza mkuluyo pamodzi ndi anthu ake makumi asanu aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nayankha Eliya, nanena nao, Ndikakhala ine munthu wa Mulungu, utsike moto wakumwamba, nunyeketse iwe ndi makumi asanu ako. Pamenepo moto wa Mulungu unatsika kumwamba nunyeketsa iye ndi makumi asanu ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Eliya anayankha kuti, “Ngati ndine munthu wa Mulungu, moto utsike kuchokera kumwamba, ukupsereze iwe pamodzi ndi anthu ako makumi asanuwo!” Pomwepo moto unatsikadi kuchokera kumwamba ndipo unapsereza mtsogoleriyo pamodzi ndi anthu akewo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nayankha Eliya, nanena nao, Ndikakhala ine munthu wa Mulungu, utsike mota wakumwamba, nunyeketse iwe ndi makumi asanu ako. Pamenepo mota wa Mulungu unatsika kumwamba nunyeketsa iye ndi makumi asanu ace.