2 Kings 1:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu ija idatumanso mkulu wina wachitatu pamodzi ndi ankhondo ake makumi asanu. Koma mkulu wachitatu uja adapita nakagwada pamaso pa Eliya, nampempha kuti, “Inu munthu wa Mulungu, chonde ndikukupemphani kuti musandiwononge ineyo pamodzi ndi anthu anga makumi asanuŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anabwerezanso kutuma mtsogoleri wachitatu ndi makumi asanu ake. Nakwera mtsogoleri wachitatuyo, nadzagwada ndi maondo ake pamaso pa Eliya, nampembedza, nanena naye, Munthu wa Mulungu inu, ndikupemphani, moyo wanga ndi moyo wa anyamata anu makumi asanu awa akhale a mtengo wake pamaso panu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mfumu inatumanso mtsogoleri wachitatu pamodzi ndi asilikali ake makumi asanu. Mtsogoleri wachitatuyu anakwera pa phiripo ndi kugwada pamaso pa Eliya. Iye anayankhula mopemba kuti, “Munthu wa Mulungu, chonde musandiwononge ineyo pamodzi ndi atumiki makumi asanu anuwa!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anabwerezaaso kutuma mtsogolen wacitatu ndi makumi asanu ace. Nakwera mtsogoleri wacitatuyo, nadzagwada ndi maondo ace pamaso pa Eliya, nampembedza, nanena naye, Munthu wa Mulungu inu, ndikupemphani, moyo wanga ndi moyo wa anyamata anu makumi asanu awa akhale a mtengo wace pamaso panu.