2 Kings 1:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Eliya adauza mfumuyo kuti “Chauta akunena kuti, ‘Pamene udaatuma amithenga kwa Baala-Zebubi, mulungu wa anthu a ku Ekeroni, kodi ndiye kuti kuno ku Israele kulibe Mulungu woti nkumpempha nzeru?’ Nchifukwa chake Chauta akuti, ‘Iweyo sudzuka pabedi wagonapo, koma ufa ndithu.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena nayo, Atero Yehova, Popeza watuma mithenga kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni, kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele kufunsira mau ake? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Eliya anawuza mfumu kuti, “Yehova akuti, ‘Chifukwa chiyani munatumiza amithenga kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni, kukafunsa ngati muti muchire? Kodi mu Israeli mulibe Mulungu woti nʼkukuyankhani funso lanu? Choncho, popeza mwachita izi, simudzadzuka pamene mwagonapo; mudzafa ndithu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena nayo, Atero Yehova, Popeza watuma mithenga kukafunsira kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni, kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israyeli kufunsira mau ace? Cifukwa cace sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.