2 Kings 1:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Ahaziya adafadi potsata mau amene Chauta adaalankhula kudzera mwa Eliya. Ndipo popeza kuti Ahaziya adaalibe mwana wamwamuna, Yoramu mbale wake adaloŵa ufumu m'malo mwake, pa chaka chachiŵiri cha ufumu wa Yehoramu, mwana wa Yosafati, mfumu ya ku Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Motero anafa monga mwa mau a Yehova adanena Eliyawo. Ndipo Yehoramu analowa ufumu m'malo mwake chaka chachiwiri cha Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda, pakuti analibe mwana wamwamuna.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero Ahaziya anafadi, monga mwa mawu a Yehova amene Eliya anayankhula. Tsono popeza Ahaziya analibe mwana, Yoramu analowa ufumu mʼmalo mwake mʼchaka chachiwiri cha Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya ku Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Motero anafa monga mwa mau a Yehova adanena Eliyawo. Ndipo Yehoramu analowa ufumu m'malo mwace caka caciwiri ca Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda, pakuti analibe mwana wamwamuna.