2 Kings 1:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mngelo wa Chauta adauza mneneri Eliya wa ku Tisibe kuti, “Nyamuka, pita ukakumane ndi amithenga a mfumu ya ku Samariya, ukaŵafunse kuti, ‘Kodi ku Israele kulibe Mulungu, apa mukupita kukapempha nzeru kwa Baala-Zebubi, mulungu wa anthu a ku Ekeroni?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mthenga wa Yehova anati kwa Eliya wa ku Tisibe, Nyamuka, kwera kukomana ndi mithenga ya mfumu ya Samariya, nunene nayo, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti mukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mngelo wa Yehova anawuza Eliya wa ku Tisibe kuti, “Nyamuka, pita ukakumane ndi amithenga a mfumu ya ku Samariya ndipo ukawafunse kuti, ‘Kodi popeza kulibe Mulungu ku Israeli, nʼchifukwa chake inu mukupita kukafunsa nzeru kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mthenga wa Yehova anati kwa Eliya wa ku Tisibe, Nyamuka, kwera kukomana ndi mithenga ya mfumu ya Samariya, nunene nayo, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israyeli, kuti mukafunsira kwa Baala Zebubu mulungu wa ku Ekroni?