2 Kings 1:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo mfumuyo idatuma mkulu wina wa ankhondo ndi anthu ake makumi asanu kukagwira Eliya. Mkuluyo adapita kwa Eliya nampeza atakhala pansi pamwamba pa phiri. Adamuuza kuti, “Inu, munthu wa Mulungu, mfumu ikukulamulani kuti mutsike.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mfumu inatuma kwa iye asilikali makumi asanu ndi mtsogoleri wao. Iye nakwera kunka kwa Eliya; ndipo taonani, analikukhala pamwamba pa phiri. Ndipo analankhula naye, Munthu wa Mulungu iwe, mfumu ikuti, Tsika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo mfumu inatuma mtsogoleri wa ankhondo ndi anthu ake makumi asanu kwa Eliya. Mtsogoleriyo anapita kwa Eliya, amene anali atakhala pamwamba pa phiri, ndipo anati, “Munthu wa Mulungu, mfumu ikuti, ‘Tsikani!’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mfumu inatuma kwa iye asilikari makumi asanu ndi mtsogoleri wao. Iye nakwera kumka kwa Eliya; ndipo taonani, analikukhala pamwamba pa phiri. Ndipo analankhula naye, Munthu wa Mulungu iwe, mfumu ikuti, Tsika.