2 Kings 10:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Ahabu anali ndi zidzukulu zazimuna 70 ku Samariya. Tsono Yehu adalemba makalata naŵatumiza ku Samariya kwa olamulira mzindawo, kwa akuluakulu ndiponso kwa anthu amene ankalera zidzukulu za Ahabu kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ahabu anali nao ana amuna makumi asanu ndi awiri m'Samariya. Nalemba akalata Yehu, natumiza ku Samariya kwa akulu a Yezireele, ndiwo akuluakulu, ndi iwo adalera ana a Ahabu, ndi kuti,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Ahabu anali ndi ana aamuna 70 a ku Samariya. Ndipo Yehu analemba makalata nawatumiza ku Samariya kwa atsogoleri a mu mzinda wa Yezireeli, kwa akuluakulu ndiponso kwa amene ankalera ana a Ahabu, nati,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ahabu anali nao ana amuna makumi asanu ndi awiri m'Samariya. Nalemba akalata Yehu, natumiza ku Samariya kwa akulu a Yezreeli, ndiwo akulu akulu, ndi iwo adalera ana a Ahabu, ndi kuti,