2 Kings 10:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
adakumana ndi abale ake a Ahaziya mfumu ya Yuda. Adaŵafunsa kuti, “Nanga inunso ndinu yani?” Iwo adayankha kuti, “Ndife abale a malemu Ahaziya, ndipo tidabwera kudzacheza ndi ana a mfumu Ahabu, ndiponso ana a mfumukazi Yezebele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehu anakomana nao abale a Ahaziya mfumu ya Yuda, nati, Ndinu ayani? Nati iwo, Ife ndife abale a Ahaziya, tilikutsika kulonjera ana a mfumu, ndi ana a nyumba yaikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehu anakumana ndi abale ena a Ahaziya mfumu ya Yuda nawafunsa kuti, “Kodi ndinu yani?” Iwo anayankha kuti, “Ndife abale ake a Ahaziya, ndipo tabwera kulonjera banja la mfumu ndi ana a mfumukazi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehu anakomana nao abale a Ahaziya mfumu ya Yuda, nati, Ndinu ayani? Nati iwo, Ife ndife abale a Ahaziya, tirikutsika kulankhulira ana a mfumu, ndi ana a nyumba yaikuru.