2 Kings 10:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yehu adati, “Atengeni amoyo.” Ndipo adaŵatenga amoyo, nakaŵaphera ku chitsime cha ku malo aja a abusaŵa, anthu okwanira 42. Sadasiyepo ndi mmodzi yemwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati iye, Agwireni amoyo. Nawagwira amoyo, nawapha ku dzenje la nyumba yosengera, ndiwo amuna makumi anai mphambu awiri; sanasiye ndi mmodzi yense.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehu analamula kuti, “Atengeni amoyo!” Choncho anawatenga amoyo ndipo anakawaphera ku chitsime cha ku malo otchedwa Beti-Ekedi wa abusa; anthu onse 42. Iye sanasiyepo ndi mmodzi yemwe wamoyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati iye, Agwireni amoyo. Nawagwira amoyo, nawapha ku dzenje la nyumba yosengera, ndiwo amuna makumi anai mphambu awiri; sanasiya ndi mmodzi yense.