2 Kings 10:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atachoka kumeneko, Yehu adakumana ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu akudzamchingamira. Tsono adamlonjera namuuza kuti, “Kodi maganizo ako akugwirizana ndi maganizo anga, monga momwe maganizo anga akugwirizanirana ndi ako?” Yehonadabu adayankha kuti, “Inde, zathu nzimodzi.” Yehu adati, “Ngati ndi momwemodi, gwire dzanja.” Yehonadabuyo adapereka dzanja lake, Yehu nkumgwira dzanja namkweza pa galeta lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atachoka pamenepo, anakomana naye Yehonadabu mwana wa Rekabu wakudzamchingamira; namlonjera, nanena naye, Mtima wako ngwoongoka kodi, monga mtima wanga uvomerezana nao mtima wako? Nati Yehonadabu, Momwemo. Ukatero undipatse dzanja lako. Nampatsa dzanja lake, namkweretsa pali iye pagaleta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehu atachoka kumeneko anakumana ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu, amene amabwera kudzakumana naye. Yehu anamulonjera nati kwa iye, “Kodi mtima wako uli bwino monga momwe mtima wanga ugwirizana nawo mtima wako?” Yehonadabu anayankha kuti, “Inde ndikugwirizana nawe.” Yehu anati, “Ngati ndi choncho, gwire dzanja.” Ndipo iye anaterodi, ndipo Yehu anamugwira dzanja namulowetsa mʼgaleta lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atacoka pamenepo, anakomana naye Yehonadabu mwana wa Rekabu wakudzamcingamira; namlankhula, nanena naye, Mtima wako ngwoongoka kodi, monga mtima wanga ubvomerezana nao mtima wako? Nati Yehonadabu, Momwemo. Ukatero undipatse dzanja lako. Nampatsa dzanja lace, namkweretsa pali iye pagareta.