2 Kings 10:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atafika ku Samariya, Yehu adapha onse amene adatsalako a banja la Ahabu, mpaka adaŵapulula onse, potsata mau a Chauta amene Eliya adaŵalankhula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anafika ku Samariya, nakantha onse otsala a Ahabu m'Samariya, mpaka adamuononga monga mwa mau a Yehova adanenawo kwa Eliya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehu atafika ku Samariya, anapha onse amene anatsala a mʼbanja la Ahabu ku Samariya; anawawonongeratu potsata mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa Eliya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anafika ku Samariya, nakantha onse otsala a Ahabu m'Samariya, mpaka adamuononga monga mwa mau a Yehova adanenawo kwa Elisa.