2 Kings 10:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake tsono itanireni aneneri onse a Baala, onse amene amapembedza Baalayo, pamodzi ndi ansembe ake onse. Pasasoŵeke ndi mmodzi yemwe, poti ndili ndi nsembe yaikulu yoti ndiipereke kwa Baala. Amene asoŵeke, adzaphedwa.” Koma Yehu adachita zimenezi mochenjera, kuti aononge onse amene ankapembedza Baala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mundiitanire tsono adze kwa ine aneneri onse a Baala, ompembedza onse, ndi ansembe ake onse, asasowe mmodzi; pakuti ndili nayo nsembe yaikulu yochitira Baala; aliyense wosapenyekapo sadzakhala ndi moyo. Koma Yehu anachichita monyenga, kuti akaononge otumikira Baala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano itanani aneneri a Baala onse, atumiki ake onse ndi ansembe ake onse. Pasapezeke ndi mmodzi yemwe wotsala chifukwa ine ndidzapereka nsembe yayikulu kwa Baala. Aliyense amene alephere kubwera adzaphedwa.” Koma Yehu anachita zimenezi mwachinyengo ndi cholinga choti awononge atumiki onse a Baala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mundiitanire tsono adze kwa ine aneneri onse a Baala, ompembedza onse, ndi ansembe ace onse, asasowe mmodzi; pakuti ndiri nayo nsembe yaikuru yocitira Baala; ali yense wosapenyekapo sadzakhala ndi moyo. Kama Yehu anacicita monyenga, kuti akaononge otumikira Baala.