2 Kings 10:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yehu adatumiza mau ku dziko lonse la Israele, ndipo onse amene ankapembedza Baala adabweradi, kotero kuti sadatsalepo ndi mmodzi yemwe. Onsewo adaloŵa m'nyumba ya Baala, ndipo anthu adachita kuti thothotho m'nyumbamo. Sipadatsale malo mpang'ono pomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehu anatumiza kwa Aisraele onse, nadza otumikira Baala onse, wosatsala ndi mmodzi yense wosafika. Nalowa m'nyumba ya Baala; ndi nyumba ya Baala inadzala phaa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Yehu anatumiza mawu ku dziko lonse la Israeli ndipo atumiki onse a Baala anabwera; palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala. Iwo anadzaza nyumba ya Baala. Nyumbayo inadzaziratu kuchokera ku khoma lina mpaka ku khoma lina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehu anatumiza kwa Aisrayeti onse, nadza otumikira Baala onse, wosatsala ndi mmodzi yense wosafika. Nalowa m'nyumba ya Baala; ndi nyumba ya Baala inadzala pha.