2 Kings 10:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yehu adaloŵa m'nyumba ya Baala pamodzi ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu. Ndipo adauza anthu aja opembedza Baalaŵa kuti: “Yang'anani bwino, ndipo muwone kuti pasakhale mtumiki wa Chauta pano pakati panupa, koma opembedza Baala okhaokha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nalowa Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu m'nyumba ya Baala, nati kwa otumikira Baala, Mufunefune, nimuone asakhale nanu muno otumikira Yehova, koma otumikira Baala okha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu analowa mʼnyumba ya Baala. Yehu anawawuza atumiki a Baala kuti, “Yangʼanitsitsani ndipo muone kuti muno musapezeke atumiki a Yehova, koma mukhale atumiki okhawo a Baala.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nalowa Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu m'nyumba ya Baala, nati kwa otumikira Baala, Mufunefune, nimuone asakhale nanu muno otumikira Yehova, koma otumikira Baala okha.