2 Kings 10:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yehu adaloŵa kukapereka nsembe zopsereza. Koma Yehu anali ataika anthu 80 panja naŵauza kuti, “Adzaphedwa amene athaŵitse aliyense mwa anthu amene ndikupatseni kuti muŵapheŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nalowa iwo kupereka nsembe zophera ndi nsembe zopsereza. Koma Yehu adadziikira kubwalo amuna makumi asanu ndi atatu, nati, Munthu akalola wina wa anthuwa ndilikuwaika m'manja mwanu apulumuke, moyo wake kulipa moyo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Yehu analowa kukapereka nsembe zina ndi nsembe zopsereza. Nthawi iyi nʼkuti Yehu atayika anthu 80 kunja kwa nyumbayo ndi chenjezo lakuti, “Ngati wina aliyense wa inu adzathawitsa wina aliyense wa anthu amene ndayika kuti muziwayangʼanira, munthu woteroyo adzaphedwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nalowa iwo kupereka nsembe zophera ndi nsembe zopsereza. Koma Yehu adadziikira kubwalo amuna makumi asanu ndi atatu, nati, Munthu akalola wina wa anthuwa ndirikuwaika m'manja mwanu apulumuke, moyo wace kulipa moyo wace.