2 Kings 10:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yehu uja atangomaliza kupereka nsembe yopsereza ija, adauza asilikali ake ndi akapitao ao kuti: “Loŵani muŵaphe! Asapulumukepo ndi mmodzi yemwe.” Iwo adaloŵadi, nkukapha onse amene anali m'menemo, naponya mitembo yao panja. Adakaloŵanso m'chipinda cham'kati cha nyumba ya Baala ija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, atatsiriza kupereka nsembe yopsereza, Yehu anati kwa otumikira ndi atsogoleri, Lowani, akantheni; asatuluke ndi mmodzi yense. Nawakantha ndi lupanga lakuthwa; ndi otumikira ndi atsogoleri anawataya kubwalo, namuka kumudzi wa nyumba ya Baala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehu atangotsiriza kupereka nsembe yopsereza, analamula alonda ndi akulu a ankhondo kuti, “Lowani ndipo mukawaphe ndipo musalole kuti wina athawe.” Choncho iwo anawapha ndi lupanga. Alonda ndi akulu a ankhondo anaponya mitembo ya anthuwo panja ndipo anakalowa mʼkati mwenimweni mwa nyumba ya Baala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, atatsiriza kupereka nsembe yopsereza, Yehu anati kwa otumikira ndi atsogoleri, Lowani, akantheni; asaturuke ndi mmodzi yense. Nawakantha ndi lupanga lakuthwa; ndi otumikira ndi atsogoleri anawataya kubwalo, namuka ku mudzi wa nyumba ya Baala.