2 Kings 10:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yehuyo sadaleke kwenikweni zoipa zimene ankachita mfumu Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene ankachimwitsa nazo Aisraele. Sadaleke kupembedza zifanizo zagolide za anaang'ombe zimene zinali ku Betele ndi ku Dani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yehu sanazileke zoipa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Israele, ndizo anaang'ombe agolide okhala m'Betele ndi m'Dani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehuyo sanaleke machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati amene anachimwitsa nawo Israeli kupembedza mafano a golide a ana angʼombe ku Beteli ndi ku Dani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yehu sanazileka zoipa za Yerobiamu mwana wa Nebati, zimene adacimwitsa nazo Israyeli, ndizo ana a ng'ombe agolidi okhala m'Beteli ndi m'Dani.