2 Kings 10:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Chauta adauza Yehu kuti: “Chifukwa choti wachita zondikomera Ine, poononga banja la Ahabu monga momwe ndinkafunira, ana ako adzakhala pa mpando waufumu wa Israele mpaka mbadwo wachinai.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Yehu, Popeza wachita bwino, pochita choongoka pamaso panga, ndi kuchitira nyumba ya Ahabu monga mwa zonse zinali m'mtima mwanga, ana ako a ku mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anati kwa Yehu, “Chifukwa wachita bwino pokwaniritsa kuchita zabwino pamaso panga ndipo wachitira banja la Ahabu zonse zimene zinali mʼmaganizo anga, zidzukulu zako zidzakhala pa mpando waufumu wa Israeli mpaka mʼbado wachinayi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Yehu, Popeza wacita bwino, pocita coongoka pamaso panga, ndi kucitira nyumba ya Ahabu monga mwa zonse zinali m'mtima mwanga, ana ako a ku mbadwo wacinai adzakhala pa mpando wacifumu wa Israyeli.