2 Kings 10:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adayambira ku Yordani chakuvuma, nakafika ku Aroere pafupi ndi chigwa cha Arinoni. Dziko limeneli lidaphatikiza madera onse a Giliyadi ndi Basani, kumene zinkakhala zidzukulu za Gadi, Rubeni ndi Manase.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuyambira ku Yordani kum'mawa, dziko lonse la Giliyadi, la Agadi, ndi la Arubeni, ndi Amanase, kuyambira ku Aroere, ndiwo kumtsinje Arinoni, ndilo Giliyadi ndi Basani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kuyambira kummawa kwa Yorodani, dziko lonse la Giliyadi (chigawo cha Gadi, Rubeni ndi Manase), kuchokera ku Aroeri pafupi ndi chigwa cha Arinoni kudutsa Giliyadi mpaka ku Basani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuyambira ku Yordano kum'mawa, dziko lonse la Gileadi, la Agadi, ndi la Arubeni, ndi Amanase, kuyambira ku Aroeri, ndiwo kumtsinje Arinoni, ndilo Gileadi ndi Basana.