2 Kings 10:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero woyang'anira nyumba ya mfumu ndiponso wina woyang'anira mzinda, pamodzi ndi akuluakulu, kudzanso amene ankalera anawo, adatumiza mau kwa Yehu kuti, “Ife ndife anthu anu, ndipo tidzachita zonse zimene mutiwuze. Sitidzaika wina aliyense kuti akhale mfumu. Muchite zonse zimene zikukomereni.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye wakuyang'anira nyumba, ndi iye wakuyang'anira mudzi, ndi akuluakulu, ndi iwo akulera anawo, anatumiza kwa Yehu, ndi kuti, Ife ndife akapolo anu ndi zonse mutiuza tidzachita; sitidzalonga munthu yense mfumu; chokomera pamaso panu chitani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho woyangʼanira nyumba ya mfumu, bwanamkubwa wa mzinda, akuluakulu ena ndiponso olera anawo anatumiza uthenga uwu kwa Yehu: “Ife ndife atumiki anu ndipo tidzachita chilichonse chomwe mutiwuze. Sitidzasankha munthu wina aliyense kukhala mfumu ndipo chitani chimene mukuganiza kuti nʼchabwino kwa inu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye wakuyang'anira nyumba, ndi iye wakuyang'anira mudzi, ndi akulu akulu, ndi iwo akulera anawo, anatumiza kwa Yehu, ndi kuti, Ife ndife akapolo anu ndi zonse mutiuza tidzacita; sitidzalonga munthu yense mfumu; cokomera pamaso panu citani.