2 Kings 10:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yehu adaŵalemberanso kalata yachiŵiri kuti, “Ngati muli pambuyo panga, ndipo ngati muli okonzeka kundimvera, mudule mitu ya ana a mbuyanu, mudze nayo kwa ine ku Yezireele maŵa nthaŵi yonga yomwe ino.” Ndiye kuti zidzukulu za mfumu 70 zija zinkaleredwa ndi akuluakulu amumzinda aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nawalembera kalata kachiwiri, nati, Mukakhala a ine ndi kumvera mau anga, tengani mitu ya amunawo ana a mbuye wanu, ndi kundidzera ku Yezireele mawa dzuwa lino. Koma ana a mfumu ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, anakhala ndi anthu omveka m'mudzi, amene anawalera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehu anawalembera kalata yachiwiri yonena kuti, “Ngati inu muli mbali yanga ndi kuti mudzandimvera, mudule mitu ya ana a mbuye wanu ndipo mubwere nayo kwa ine ku Yezireeli mawa nthawi ngati yomwe ino.” Tsono ana a mfumu onse 70 anali pamodzi ndi akuluakulu a mu mzindamo, amene ankawalera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nawalembera kalata kaciwiri, nati, Mukakhala a ine ndi kumvera mau anga, tengani mitu va amunawo ana a mbuyewanu, ndi kundidzera ku Yezreeli mawa dzuwa lino. Koma ana a mfumu ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, anakhala ndi anthu omveka m'mudzi, amene anawalera.