2 Kings 10:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye akuluakuluwo atalandira kalata ija, adagwira zidzukulu za mfumuzo nkuzipha, 70 zonsezo, naika mitu yao m'madengu, nkuitumiza kwa Yehu ku Yezireele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, powafika kalatayo, anatenga ana a mfumu, nawapha amuna makumi asanu ndi awiri, naika mitu yao m'madengu, naitumiza kwa iye ku Yezireele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kalatayo itafika, anthuwo anatenga ana a mfumu 70 aja ndi kuwapha onse. Anayika mitu yawo mʼmadengu ndi kuyitumiza ku Yezireeli kwa Yehu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, powafika kalatayo, anatenga ana a mfumu, nawapha amuna makumi asanu ndi awiri, naika mitu yao m'mitanga, naitumiza kwa iye ku Yezreeli.