2 Kings 10:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'maŵa mwake atatuluka, Yehu adapitako nauza anthu onse kuti, “Inu sindinu ochimwa ai. Wochimwa ndine, popeza kuti ndidachita chiwembu mbuyanga, ndipo ndidamupha. Koma adapha anthu onseŵa ndani?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali m'mawa, iye anatuluka, naima, nati kwa anthu onse, Muli olungama inu, taonani, ndinapandukira mbuye wanga ndi kumupha; koma awa onse anawakantha ndani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmawa mwake Yehu anatuluka. Iye anayimirira pamaso pa anthu onse ndipo anati, “Inu ndinu osalakwa. Ndine amene ndinachita chiwembu mbuye wanu ndi kumupha, koma kodi wapha anthu onsewa ndani?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali m'ma wa, iye anaturuka, naima, nati kwa anthu onse, Muli olungama inu, taonani, ndinapandukira mbuye wanga ndi kumupha; koma awa onse anawakantha ndani?