2 Kings 11:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ataliya, mai wake wa Ahaziya, ataona kuti mwana wake wafa, adanyamuka nakaononga onse a pa banja laufumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene Ataliya make wa Ahaziya anaona kuti mwana wake wafa, ananyamuka, naononga mbeu yonse yachifumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ataliya amayi ake a Ahaziya ataona kuti mwana wawo wafa, ananyamuka nakawononga banja lonse la mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene Ataliya mace wa Ahaziya anaona kuti mwana wace wafa, ananyamuka, naononga mbeu yonse yacifumu.