2 Kings 11:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka adaŵatulutsira mwana wa mfumu, namuveka chisoti chaufumu, nkumupatsa buku la malamulo, ndipo adamdzoza namlonga ufumu. Anthu adamuwombera m'manja nkunena mofuula kuti, “Amfumu akhale ndi moyo wautali.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atatero, anatulutsa mwana wa mfumu, namuika korona, nampatsa buku la umboni, namlonga ufumu, namdzoza, naomba m'manja, nati, Mfumu ikhale ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehoyada anatulutsa mwana wa mfumuyo namuveka chipewa chaufumu ndipo anamupatsa Buku la Chipangano ndi kumuyika kukhala mfumu. Iwo anamudzoza ndipo anthu anamuwombera mʼmanja akufuwula kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atatero, anaturutsa mwana wa mfumu, namuika korona, nampatsa buku la umboni, namlonga ufumu, namdzoza, naomba m'manja, nati, Mfomu ikhale ndi movo.