2 Kings 11:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atayang'ana, adaona mfumu itaima pa nsanja yake potsata mwambo wachifumu, atsogoleri ndi anthu oimba malipenga ali pafupi ndi mfumuyo. Anthu onse am'deralo ankakondwa, namaimba malipenga. Pamenepo Ataliyayo adang'amba zovala zake, ndipo mofuula adati, “Akundiwukira! Akundiwukira!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
napenya, ndipo taonani, mfumu ili chilili pachiundo, monga ankachita, ndi atsogoleri ndi amalipenga pali mfumu; nakondwerera anthu onse a m'dziko, naomba malipenga. Pamenepo Ataliya anang'amba zovala zake, nafuula Chiwembu, Chiwembu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayangʼana naona mfumu itayima pa chipilala, potsata mwambo waufumu. Atsogoleri a asilikali ndi oyimba malipenga anali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a mʼderalo ankasangalala ndi kuyimba malipenga. Pamenepo Ataliya anangʼamba mkanjo wake nafuwula kuti, “Kuwukira! Kuwukira!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
napenya, ndipo taonani, mfumu iri ciriri paciundo, monga adafocita, ndi atsogoleri ndi amalipenga pali mfomu; nakondwerera anthu onse a m'dziko, naomba malipenga. Pamenepo Ataliya anang'amba zobvala zace, napfuula, Ciwembu, Ciwembu.