2 Kings 11:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono wansembe Yehoyada adalamula atsogoleri a gulu lankhondo aja kuti, “Mtulutseni ameneyu pakati pa mizere mwandandayo. Ndipo aliyense amene amtsate, mumuphe ndi lupanga.” Wansembeyo adaanenadi kuti, “Musamphere m'Nyumba ya Chauta ai.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yehoyada wansembe analamulira atsogoleri a mazana oyang'anira khamu, nanena nao, Mumtulutse mkaziyo pabwalo pakati pa mipambo; womtsata iye mumuphe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Asaphedwe m'nyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe Yehoyada analamula atsogoleri a asilikali 100 amene amayangʼanira asilikaliwo kuti, “Mutulutseni ameneyo pakati panu ndipo muphe ndi lupanga aliyense amene adzamutsata.” Pakuti nʼkuti wansembeyo atanena kuti, “Ataliyayo asaphedwere mʼNyumba ya Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yehoyada wansembe analamulira atsogoleri a mazana oyang'anira khamu, nanena nao, Mumturutse mkaziyo pabwalo pakati pa mipambo; womtsata iye mumuphe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Asaphedwe m'nyumba ya Yehova.