2 Kings 11:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho anthu onse a m'dzikomo adapita ku nyumba ya Baala nakaigwetsa. Maguwa ake ndi mafano ake adaŵaphwanyaphwanya. Kenako adapha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwa pomwepo. Tsono wansembe Yehoyada adaika alonda ku Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Namuka anthu onse a m'dzikomo kunyumba ya Baala, naigumula; maguwa ake a nsembe ndi mafano ake anawaswaiswa, napha Matani wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe. Ndipo wansembeyo anaika oyang'anira nyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onse a mʼdzikomo anapita ku nyumba ya Baala nakayigwetsa. Iwo anaphwanya kotheratu maguwa ansembe ndi mafano ake ndipo anapha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwa pomwepo. Pamenepo wansembe Yehoyada anasankha oyangʼanira Nyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Namuka anthu onse a m'dzikomo ku nyumba ya Baala, naigumula; maguwa ace a nsembe ndi mafano ace anawaswaiswa, napha Matana wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe. Ndipo wansembeyo anaika oyang'anira nyumba ya Yehova.