2 Kings 11:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake iyeyo adandanditsa atsogoleri a ankhondo, asilikali olonda mfumu, alonda a nyumba ya mfumu, ndi anthu onse a m'dzikomo. Onsewo adaperekeza mfumu kuchokera ku Nyumba ya Chauta, nadzera ku chipata cha alonda mpaka kukafika ku nyumba ya mfumu. Pomwepo Yowasi adakhala pa mpando waufumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Napita nao atsogoleri a mazana, ndi opha anthu, ndi otumikira, ndi anthu onse a m'dziko; ndipo iwo anatsika nayo mfumu kunyumba ya Yehova, nadzera njira ya chipata cha otumikira, kunka kunyumba ya mfumu. Nakhala iye pa chimpando cha mafumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anatenga atsogoleri a asilikali 100 aja, alonda olonda nyumba yaufumu pamodzi ndi anthu onse a mʼdzikomo ndipo onse pamodzi anayitulutsa mfumu mʼNyumba ya Yehova ndi kukalowa ku nyumba yaufumu podzera pa chipata cha alonda. Ndipo mfumuyo inakhala pa mpando wake waufumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Napita nao atsogoleri a mazana, ndi opha anthu, ndi otumikira, ndi anthu onse a m'dziko; ndipo iwo anatsika nayo mfumu ku nyumba ya Yehova, nadzera njira ya cipata ca otumikira, kumka ku nyumba ya mfomu. Nakhala Iye pa cimpando ca mafumu.