2 Kings 11:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, adatenga Yowasi, mwana wa Ahaziya. Adachita momuba, kumchotsa pakati pa ana aamuna a mfumu amene ankati aŵaphewo. Adamuika m'chipinda china chogona cha m'Nyumba ya Chauta pamodzi ndi mlezi wake. Motero adamubisa mwanayo, kubisira Ataliya, kotero kuti sadaphedwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yehoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m'chipinda chogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namusunga kutali ndi ana a mfumu amene ankati awaphewo. Anamuyika iye pamodzi ndi mlezi wake mʼchipinda chogona chamʼkati kubisira Ataliya kotero iye sanaphedwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yoseba mwana wa mfumu Yoramu, mlongo wace wa Ahaziya, anatenga Yoasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu akuti aphedwe, iye ndi mlezi, nawaika m'cipinda cogonamo; nambisira Ataliya, ndipo sanaphedwa.