2 Kings 11:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri, wansembe Yehoyada adatumiza mau kukaitana atsogoleri a asilikali olonda mfumu ndipo a alonda a nyumba yaufumu. Adabwera nawo kwa Yehoyada ku Nyumba ya Chauta. Tsono adapangana nawo chipangano ndipo adaŵalumbiritsa m'Nyumba ya Chauta. Kenaka adaŵaonetsa mwana wamwamuna wa mfumu uja,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a mazana a opha anthu, ndi a otumikira, nabwera nao kwa iye kunyumba ya Yehova, napangana nao, nawalumbiritsa m'nyumba ya Yehova, nawaonetsa mwana wa mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mʼchaka chachisanu ndi chiwiri, Yehoyada anatumiza mawu kukayitana atsogoleri olamulira asilikali 100 olondera mfumu ndiponso alonda olonda nyumba yaufumu ndipo anabwera nawo mʼNyumba ya Yehova. Iye anapangana nawo pangano ndipo anawalumbiritsa mʼnyumba ya Yehova. Kenaka anawaonetsa mwana wamwamuna wa mfumu uja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma caka cacisanu ndi ciwiri Yehoyada anaitanitsa atsogoleri a mazana a opha anthu, ndi a otumikira, nabwera nao kwa iye ku nyumba ya Yehova, napangana nao, nawalumbiritsa m'nyumba ya Yehova, nawaonetsa mwana wa mfumu.