2 Kings 12:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi zonse ankati akaona kuti m'bokosimo muli ndalama zambiri, mlembi wa mfumu ndi mkulu wa ansembe ankabwera kudzaŵerenga ndi kumanga m'matumba ndalama zimene zinali m'Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakuona kuti ndalama zidachuluka m'bokosimo, anakwerako mlembi wa mfumu, ndi mkulu wa ansembe, nazimanga m'matumba, naziyesa ndalama zopereka m'nyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi zonse akaona kuti mʼbokosimo muli ndalama zambiri, mlembi wa mfumu ndi mkulu wa ansembe ankabwera ndipo ankawerenga ndalama zomwe anthu ankabwera nazo ku Nyumba ya Yehova ndi kuziyika mʼmatumba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakuona kuti ndarama zidacuruka m'bokosimo, anakwerako mlembi wa mfumu, ndi mkuru wansembe, nazimanga m'matumba, naziyesa ndalama zopereka m'nyumba ya Yehova.