2 Kings 12:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndalamazo ataziyesa, ankazipereka kwa akapitao okonzetsa Nyumba ya Chauta aja. Iwowo ankalipira amisiri a matabwa ndi amisiri omanga nyumba, amene ankagwira ntchito yokonza Nyumba ya Chautayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Napereka ndalama zoyesedwa m'manja mwa iwo akuchita ntchitoyi, akuyang'anira nyumba ya Yehova; ndipo iwo analipira nazo amisiri a mitengo ndi omanga, akugwira ntchito ya pa nyumba ya Yehova,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ankati akadziwa kuti ndalamazo zilipo zingati, ankazipereka kwa anthu amene ankayangʼanira ntchito yokonza nyumbayo. Ndalamazo ankalipira anthu amene ankagwira ntchito yokonza Nyumba ya Yehova, amisiri a matabwa ndi amisiri omanga nyumba,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Napereka ndarama zoyesedwa m'manja mwa iwo akucita nchitoyi, akuyang'anira nyumba ya Yehova; ndipo iwo analipira nazo amisiri a mitengo ndi omanga, akugwira nchito ya pa nyumba ya Yehova,