2 Kings 12:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mabeseni asiliva a ku Nyumba ya Chauta, ngakhale mbano, mbale, malipenga, ziŵiya zagolide ndi zasiliva, sadagule ndi ndalama zimene zinkabwera ku Nyumba ya Chauta,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma sanapangire nyumba ya Yehova mbale zasiliva, mbano, mbale zowazira, malipenga, zotengera zilizonse zagolide, kapena zotengera zilizonse zasiliva, kuzipanga ndi ndalama adabwera nazo kunyumba ya Yehova;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndalama zomwe anthu ankabwera nazo ku nyumbayo sanagulire siliva wopangira mabeseni, zozimitsira nyale, mbale zowazira magazi, malipenga kapena ziwiya zina zilizonse zagolide kapena zasiliva za ku Nyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma sanapangira nyumba ya Yehova mbale zasiliva, mbano, mbale zowazira, malipenga, zotengera ziri zonse zagolidi, kapena zotengera ziri zonse zasiliva, kuzipanga ndi ndarama adabwera nazo ku nyumba ya Yehova;