2 Kings 12:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu amene ankaŵapatsa ndalama zolipirira antchito okonza Nyumbawo, sankaŵafunsa kuti afotokoze za kamwazidwe ka ndalamazo, popeza kuti anali anthu okhulupirika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo sanawerengere anthu, amene anapereka ndalamazi m'manja mwao kuti apatse ogwira ntchito; popeza anachita mokhulupirika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma sanawafunse kuti afotokoze kagwiritsidwe ntchito ka ndalama zolipira amene ankagwira ntchito, chifukwa anthuwo ankagwira ntchitoyo mokhulupirika kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo sanawerengera anthu, amene anapereka ndaramazi m'manja mwao kuti apatse ogwira nchito; popeza anacita mokhulupirika.