2 Kings 12:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo Hazaele, mfumu ya ku Siriya, adathira nkhondo mzinda wa Gati, ndipo adaulanda mzindawo. Kenaka Hazaele adatsimikiza mtima kuti akathire nkhondo ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Hazaele mfumu ya Aramu anakwera, nathira nkhondo pa Gati, naulanda, nalunjikitsa nkhope yake kukwera ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi imeneyo, Hazaeli, mfumu ya Aramu anapita kukathira nkhondo mzinda wa Gati nawulanda. Kenaka Hazaeli anatembenuka kupita kukathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Hazaeli mfumu ya Aramu anakwera, nathira nkhondo pa Gati, naulanda, nalunjikitsa nkhope yace kukwera ku Yerusalemu.