2 Kings 12:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yowasi mfumu ya ku Yuda adatenga zopereka zonse zopatulika zimene Yehosafati, Yehoramu ndi Ahaziya, makolo ake, mafumu a ku Yuda, adazipereka kwa Mulungu pamodzi ndi mphatso zakezake zopatulika, kudzanso golide yense amene adampeza m'nyumba zosungira chuma cha ku Nyumba ya Chauta ndi cha ku nyumba ya mfumu. Zonsezo adazitumiza ngati mphatso zopepesera Hazaele mfumu ya ku Siriya. Tsono Hazaele adazilandira nachokako ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yowasi mfumu ya Yuda anatenga zopatulika zonse adazipatula Yehosafati, ndi Yehoramu, ndi Ahaziya, makolo ake, mafumu a Yuda, ndi zopatulika zakezake, ndi golide yense anampeza pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi cha nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Hazaele mfumu ya Aramu; motero anabwerera kuchoka ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yowasi mfumu ya Yuda anatenga zinthu zonse zopatulika zomwe anazipatula Yehosafati, Yehoramu, ndi Ahaziya abambo ake, mafumu a Yuda ndi mphatso zonse zomwe iye mwini anazipereka: golide yense amene anapezeka mʼnyumba yosungiramo chuma cha mʼnyumba ya Yehova ndi zomwe zinali mʼnyumba ya mfumu, nazipereka kwa Hazaeli mfumu ya Aramu. Pamenepo iye anachoka ku Yerusalemuko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yoasi mfumu ya Yuda: anatenga zopatulika zonse adazipatula Yehosafati, ndi Yoramu, ndi Ahaziya, makolo ace, mafumu a Yuda, ndi zopatulika zace zace, ndi golidi yense anampeza pa cuma ca nyumba ya Yehova, ndi ca nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Hazaeli mfumu ya Aramu; motero anabwerera kucoka ku Yerusalemu.