2 Kings 12:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yosakara, mwana wa Simeati, ndi Yehozabadi, mwana wa Somere, ndiwo amene adachita zimenezi. Ndipo adakamuika m'manda momwe adaikidwa makolo ake mu mzinda wa Davide. Tsono Amaziya, mwana wake, adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Yozakara mwana wa Simeati, ndi Yehozabadi mwana wa Somere, anyamata ake, anamkantha, nafa iye; ndipo anamuika kwa makolo ake m'mudzi wa Davide; ndi Amaziya mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yozakara mwana wa Simeati ndi Yehozabadi mwana wa Someri atumiki ake anamukantha nafa. Ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Amaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Yozakara mwana wa Simeati, ndi Yosabadi mwana wa Someri, anyamata ace, anamkantha, nafa iye; ndipo anamuika kwa makolo ace m'mudzi wa Davide; ndi Amaziya mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.