2 Kings 12:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi ina mfumu Yowasi adauza ansembe kuti, “Musunge bwino ndalama zonse zimene zimaperekedwa ngati zopereka zopatulika ku Nyumba ya Chauta, ndiye kuti ndalama za msonkho wa munthu aliyense, ndiponso ndalama zimene munthu amapereka mwaufulu ku Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yowasi anati kwa ansembe, Landirani ndalama zonse za zinthu zopatulika azibwera nazo kunyumba ya Yehova, ndizo ndalama za otha msinkhu, ndalama za munthu aliyense monga adamuyesa, ndi ndalama zimene yense azikumbuka m'mtima mwake kuti abwere nazo kunyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yowasi anati kwa ansembe, “Tolerani ndalama zonse zimene zimaperekedwa monga chopereka chopatulika ku Nyumba ya Yehova, ndalama zonse zamsonkho wa munthu aliyense, ndalama zomwe munthu amapereka akalonjeza ndiponso ndalama zimene munthu amapereka mwaufulu ku Nyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoasi anati kwa ansembe, Landirani ndarama zonse za zinthu zopatulika azibwera nazo ku nyumba ya Yehova, ndizo ndarama za otha msinkhu, ndarama za munthu ali yense monga adamuyesa, ndi ndalama zimene yense azikumbuka m'mtima mwace kuti abwere nazo ku nyumba ya Yehova.